Eksodo 21 BL92

Lamulo la pa kapolo, ndi la pa wakupha mnzace

1 Ndipo awa ndiwo maweruzo amene uziika pamaso pao.

2 Ukagula mnyamata Mhebri, azigwira nchito zaka zisanu ndi cimodzi; koma cacisanu ndi ciwiri azituruka waufulu cabe.

3 Akalowa ali yekha azituruka ali yekha; akakhala ndi mkazi, mkazi wace azituruka naye.

4 Akampatsa mkazi mbuye wace, ndipo akambalira ana amuna ndi akazi, mkaziyo ndi ana ace azikhala a mbuye wace, ndipo azituruka ali yekha.

5 Koma mnyamatayo akanenetsa, Ndikonda mbuye wanga, mkazi wanga, ndi ana anga; sindituruka waufulu;

6 pamenepo mbuye wace azifika naye kwa oweruza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wace amboole khutu lace ndi lisungulu; ndipo iye azimgwirira nchito masiku onse.

7 Ndipo munthu akagulitsa mwana wace wamkazi akhale mdzakazi, iyeyo asaturuke monga amaturuka anyamata.

8 Akapanda kumkonda mbuye wace, amene anamtoma mwini yekha, azilola kuti amuombole; alibe mphamvu yakumgulitsa kwa anthu acilendo, popeza wacita naye monyenga.

9 Koma ngati amtomera mwana wace wamwamuna, amcitire monga kuyenera ana akazi.

10 Akamtengera mkazi wina, asacepetse cakudya cace, zobvala zace, ndi za ukwati zace zace.

11 Ndipo akapanda kumcitira izi zitatu, azituruka cabe, osaperekapo ndalama.

12 Iye amene akantha munthu kotero kuti wafa, aphedwe ndithu.

13 Koma akapanda kumlalira, koma Mulungu akalola akomane ndi mnzace, ndidzakuikirani pothawirapo iye.

14 Koma munthu akacita dala pa mnzace, kumupha monyenga; uzimcotsa ku guwa langa la nsembe, kuti afe.

15 Munthuwakukanthaatatewace, kapena amai wace, aphedwe ndithu.

16 Iye wakuba munthu, angakhale wamgulitsa, kapena akampeza m'dzanja lace, aphedwe ndithu.

Malamulo a pa wotemberera ombala ndi opweteka anzao

17 Munthu wakutemberera atate wace, kapena amai wace, aphedwe ndithu.

18 Akalimbana amuna, ndipo wina akakantha mnzace ndi mwala, kapena ndi nkhonyo, wosafa iye, koma wakhulungira pakama;

19 akaukanso, nakayendayenda pabwalo ndi ndodo yace, womkanthayo azikhala womasuka; pakutsotsa pace pokha azimbwezera, namcizitse konse.

20 Munthu akakantha mnyamata wace, kapena mdzakazi wace, ndi ndodo, ndipo akafa padzanja pace; ameneyo aliridwe ndithu.

21 Koma akakhala wosafa tsiku limodzi kapena awiri, asalirike, pakuti ndiye ndalama ya mbuye wace.

22 Akayambana amuna, nakakantha mkazi ali ndi pakati, kotero kuti abala, koma alibe kuphwetekwa; alipe ndithu, monga momwe amchulira mwamuna wa mkaziyo; apereke monga anena oweruza.

23 Koma ngati kuphweteka kukalipo, uzipereka moyo kulipa moyo,

24 diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi,

25 kutentha kulipa kutentha, bala kulipa bala, mkwapulo kulipa mkwapulo.

26 Munthu akampanda mnyamata wace, kapena mdzakazi wace, padiso, nalithudzula, azimlola amuke waufulu cifukwa ca diso lace.

27 Ndipo akagurula dzino la mnyamata wace, kapena dzino la mdzakazi wace, azimlola amuke waufulu cifukwa ca dzino lace.

28 Ng'ombe ikatunga mwamuna kapena mkazi, nafa, aiponyetu miyala ng'ombeyo, osadya nyama yace; koma mwini ng'ombeyo azimasuka.

29 Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamcenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini waceyo amuphenso.

30 Akamuikira dipo, azipereka ciombolo ca moyo wace monga mwa zonse adamuikira.

31 Ingakhale yatunga mwana wamwamuna kapena wamkazi, aicitire monga mwa ciweruzo ici.

32 Ng'ombeyo ikatunga mnyamata kapena mdzakazi, azipatsa mbuye wace ndalama za masekele a siliva makumi atatu, ndipo ng'ombeyo aiponye miyala.

Malamulo a pa cuma

33 Munthu akafukula dzenje, kapena akakumba dzenje, osalibvundikira, ndipo ikagwamo ng'ombe kapena buru,

34 mwini dzenje azilipa; azilipa ndalama kwa mwini nyamayo, koma yakufayo ndi yace.

35 Ng'ombe ya mwini ikapweteka ng'ombe ya mnzace, nifa, azigulitsa ng'ombe yamoyoyo, nagawe ndalama zace; naigawe, ndi yakufa yomweyo.

36 Kapena kudadziwika kuti ng'ombeyo ikatunga masiku adapitawo, koma osaisunga mwiniyo, azilipa ndithu, ng'ombe kulipa ng'ombe, koma yakufayo ndi yace.