Eksodo 9 BL92

Cozizwitsa cacisanu: Kalira pa zoweta

1 Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, numuuze, Atero Yehova Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire.

2 Pakuti ukakana kuwalola amuke, ndi kuwagwira cigwiritsire,

3 taona, dzanja la Yehova lidzakhala pa zoweta zako za kubusa, pa akavalo, pa aburu, pa ngamila, pa ng'ombe, ndi pa zoweta zazing'ono ndi kalira woopsa.

4 Ndipo Yehova adzasiyanitsa pakati pa zoweta za Israyeli ndi zoweta za Aigupto; kuti kasafe kanthu kali konse ka ana a Israyeli,

5 Ndipo Yehova anaika nthawi yakuti, nati, Mawa Yehova adzacita cinthu ice m'dzikomu.

6 Ndipo m'mawa mwace Yehova anacita cinthuco, ndipo zinafa zoweta zonse za m'Aigupto; koma sicinafa cimodzi conse ca zoweta za ana a Israyeli.

7 Ndipo Farao anatuma, taonani, sicidafa cingakhale cimodzi comwe ca zoweta za Aisrayeli. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalola anthu amuke.

Cozizwitsa ca 6: Zironda pa anthu ndi zoweta

8 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Tengani phulusa la ng'anjo lodzala manja; ndi Mose aliwaze kuthambo pamaso pa Farao.

9 Ndipo lidzakhala pfumbi losalala pa dziko lonse la Aigupto, ndipo lidzakhala pa anthu ndi pa zoweta ngati zironda zobuka ndi matuza, m'dziko lonse la Aigupto.

10 Ndipo anatenga phulusa la m'ng'anjo, naima pamaso pa Farao; ndi Mose analiwaza kuthambo; ndipo linakhala zironda zobuka ndi matuza pa anthu ndi pa zoweta.

11 Ndipo alembi sanakhoza kuima pamaso pa Mose cifukwa ca zirondaw; popeza panali zironda pa alembi ndi pa Aaigupto onse.

12 Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, kuti sanamvera iwo; moga Yehova adalankhula ndi Mose.

Cozizwitsa ca 7: Matalala

13 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uka oulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, akanditumikire.

14 Pakuti nthawi yino ndidzatuma miliri yanga yonse pamtima pako, ndi pa anayamata ako, ndi pa anthu ako; kuti udziwe kuti palibe wina wonga Ine pa dziko lonse lapansi.

15 Pakuti ndatambasula dzanja langa tsopano, kuti ndikupande iwe ndi anthu ako ndi mliri, ndi kuti uonoogeke pa dziko lapansi.

16 Koma ndithu cifukwa cace ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi.

17 Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke?

18 Taona, mawa monga nthawi yino ndidzabvumbitsa mbvumbi wa matalala, sipadakhala unzace m'Aigupto kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino.

19 Ndipo tsopano, tumiza, thawitsa zoweta zako ndi zonse uli nazo pabwalo; pakuti anthu onse ndi zoweta zonse zopezeka pabwalo, zosasonkhanidwa m'nyumba, matalala adzazigwera, ndipo zidzafa.

20 Iyeyu wa anyamata a Farao wakuopa mau a Yehova anathawitsira m'zinyumba anyamata ace ndi zoweta zace;

21 koma iyeyu wosasamalira mau a Yehova anasiya anyamata ndi zoweta zace kubusa.

22 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako kuthambo, kuti pakhale matalala pa dziko lonse la Aigupto, pa anthu ndi pa zoweta, ndi pa zitsamba zonse za kuthengo, m'dziko la Aigupto.

23 Pamenepo Mose anasamulira ndodo yace kuthambo, ndipo Yehova anatumiza bingu ndi matalala, ndi moto unatsikira pansi; ndipo Yehova anabvumbitsa matalala pa dziko la Aigupto.

24 Potero panali matalala, ndi mota wakutsikatsika pakati pa matalala, coopsa ndithu; panalibe cotere m'dziko lonse la Aigupto ciyambire mtundu wao.

25 Ndipo matalala anapanda m'dziko lonse la Aigupto zonse za pabwalo, kuyambira anthu kufikira zoweta; ndipo matalala anapanda zitsamba zonse za kuthengo, nathyola mitengo yonse ya kuthengo.

26 M'dziko la Goseni mokha, mokhala ana a Israyeli, munalibe matalala.

27 Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nao, Ndacimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa,

28 Pembani kwa Yehova; cifukwa akwanira ndithu mabingu a Mulungu ndi matalala; ndipo ndidzakulolani mumuke, osakhalanso.

29 Ndipo Mose ananena naye, Poturuka m'mudzi ine, ndidzasasatulira manja anga kwa Yehova; mabingu adzaleka, ndi matalala sadzakhalaponso; kuti mudziwe kuti dziko lapansi nla Yehova.

30 Koma inu ndi anyamata anu ndidziwa kuti simudzayamba kuopa nkhope ya Yehova Mulungu.

31 Ndipo thonje ndi barele zinayoyoka; pakuti barele lidafura, ndi thonje lidayamba maluwa.

32 Koma tirigu ndi rai sizinayoyoka popeza amabzala m'mbuyo.

33 Ndipo Mose anaturuka kwa Farao m'mudzi nasasatulira manja ace kwa Yehova; ndipo mabingu ndi matalala analeka, ndi mvula siinabvumbanso padziko.

34 Pamene Farao anaona kuti mvula ndi matalala ndi mabingu zidaleka anaonjezanso kucimwa, naumitsa mtima wace, iye ndi anyamata ace.

35 Potero mtima wa Farao unalimba, ndipo sanalola ana a Israyeli amuke; monga Yehova adalankhula mwa Mose.