1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Taona, ndakuika ngati Mulungu kwa Farao; ndi Aroni mkuru wako adzakhala mneneri wako.
2 Iwe uzdankhula zonse ndikulamulira; ndi Aroni mkuru wako azilankhula kwa Farao, kuti alole ana a Israyeli aturuke m'dziko lace.
3 Koma Ine ndidzaumitsa mtima wace wa Farao, ndipo ndidzacurukitsa zizindikilo ndi zozizwa zanga m'dziko la Aigupto.
4 Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aigupto, ndipo ndidzaturutsa makamu anga, anthu anga ana a Israyeli, m'dziko la Aigupto ndi maweruzo akuru.
5 Ndipo Aaigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakutambasula Ine dzanja langa pa Aigupto, ndi kuturutsa ana a Israyeli pakati pao.
6 Ndipo Mose ndi Aroni anacita monga Yehova anawalamulira, momwemo anacita.
7 Ndipo Mose anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu, ndi Aroni anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu kudza zitatu, pamene ananena ndi Farao.
8 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, ndi kuti,
9 Pamene Farao adzalankhula nanu, ndi kuti, Dzicitireni codabwiza; pamenepo uzinena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, Iponye pansi pamaso pa Farao, isanduke cinjoka,
10 Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao, nacita monga momwe Yehova adawalamulira; ndipo Aroni anaponya pansi ndodo yace pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ace, ndipo inasanduka cinjoka,
11 Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aigupto, iwonso anacita momwemo ndi matsenga ao.
12 Pakuti yense anaponya pansi ndodo yace, ndipo zinasanduka zinjoka; koma ndodoya Aroni inameza ndodo zao,
13 Koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvera iwo; monga adalankhula Yehova.
14 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Walemera mtima wa Farao, akana kulola anthu apite,
15 Muka kwa Farao m'mawa; taona, aturuka kumka kumadzi; nuime kumlinda m'mbali mwa nyanja; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m'dzanja lako.
16 Ndipo ukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri anandituma kwa inu, ndi kuti, Lola anthu anga amuke kuti anditumukire m'cipululu; koma, taona, sunamvera ndi pano.
17 Atero Yehova, Ndi ici udzadziwa kuti Ine ndine Yehova: taonani, ndidzapanda madzi ali m'nyanja ndi ndodo iri m'dzanja langa, ndipo adzasanduka mwazi.
18 Ndi nsomba ziri m'nyanja zidzafa, ndi nyanja idzanunkha; ndi Aaigupto adzacita mtima useru ndi kumwa madzi a m'nyanjamo.
19 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, nutambasule dzanja lako pa madzi a m'Aigupto, pa nyanja yao, pa ngalande zao, ndi pa matamanda ao, ndi pa matawale ao onse amadzi, kuti asanduke mwazi; mukhale mwazi m'dziko lonse la Aigupto, m'zotengera zamtengo, ndi zamwala.
20 Ndipo Mose ndi Aroni anacita monga momwe Yehova adawalamulira; nasamula ndodo, napanda madzi ali m'nyanjamo pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ace; ndipo madzi onse a m'nyanjamo anasanduka mwazi.
21 Ndi nsomba za m'nyanjamo zinafa; ndi nyanjayo inanunkha; ndipo Aaigupto sanakhoza kumwa madzi a m'nyanjamo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Aigupto.
22 Ndipo alembi a Aigupto anacita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvera iwo; monga adalankhula Yehova.
23 Ndipo Farao anatembenuka, nalowa m'nyumba yace, osasamalira ici comwe mumtima mwace.
24 Koma Aaigupto onse anakumba m'mphepete mwa nyanja kufuna madzi akumwa; pakuti sanakhoza kumwa madzi a m'nyanjamo.
25 Ndipo anafikiramasiku asanu ndi awiri atapanda nyanja Yehova.