Eksodo 23 BL92

Za mabodza ndi zonyenga

1 Usatola mbiri yopanda pace; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yocititsa ciwawa.

2 Usatsata unyinji wa anthu kucita coipa; kapena usacita umboni kumlandu, ndi kupatukira kutsata unyinji ndi kukhotetsa mlandu;

3 kapena usakometsera munthu wosauka pa mlandu wace.

4 Ukakomana ndi ng'ombe kapena buru wa mdani wako zirimkusokera, uzimbwezera izo ndithu.

5 Ukaona buru wa munthuwakudana nawe alikugona pansi ndi katundu wace, ndipo ukadaleka kuthandiza, koma uzimthandiza ndithu.

6 Usakhotetsa mlandu wa mnzako waumphawi.

7 Uzikhala kutali ndi mlandu wonama; ndipo usapha munthu wosacimwa ndi wolungama; pakuti sindidzayesa wolungama munthu woipa.

8 Usalandira cokometsera mlandu; pakuti cokometsera mlandu cidetsa maso a openya, nicisanduliza mlandu wa olungama,

9 Usampsinia mlendo; pakuti mudziwa mtima wa mlendo popeza munali alendo m'dziko la Aigupto.

Za nthawi zopumula

10 Ndipo uzibzala m'munda mwako zaka zisanu ndi cimodzi, ndi kututa zipatso zako;

11 koma caka cacisanu ndi ciwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo ndipo zotsalira iwowa zoweta za kubusa zizidye; momwemo uzicita ndi munda wako wamphesa, ndimundawakowaazitona.

12 Uzicita nchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lacisanu ndi ciwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi buru wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakaziwako ndi mlendo atsitsimuke.

13 Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusachule dzina la milungu yina; lisamveke pakamwa pako.

Za madyerero atatu m'caka

14 Muzindicitira loe madyerero katatu m'caka.

15 Uzisunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda cotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unaturuka m'Aigupto; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu;

16 ndi madyerero a masika, zipatso zoyamba za nchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi madyerero a kututa, pakutha caka, pamene ututa nchito zako za m'munda.

17 Katatu m'caka amuna onse azioneka pamaso pa Ambuye Yehova.

18 Usapereka mwazi wa nsembe yanga pamodzi ndi mkate wacotupitsa; ndi mafuta a madyerero anga asagonamo kufikira m'mawa.

19 Uzibweca nazo zoyambayamba za m'munda mwako ku nyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphike mwana wa mbuzi mu mkaka wa mace.Mulungu aloniezana nao za Kanani.

20 Taona, ndituma mthenga akutsogolere, kukusunga panjira, ndi kukufikitsa pamalo pomwe ndakonzeratu.

21 Musamalire iye, ndi kumvera mau ace; musamwawitsa mtima, pakuti sadzakhululukira zoo lakwa zanu; popeza dzina langa liri m'mtima mwace.

22 Pakuti ukamveratu mau ace, ndi kucita zonse ndizilankhula, ndidzakhala mdani wa adani ako, ndipo ndidzasautsa akusautsa iwe.

23 Pakuti mthenga wanga adzakutsogolera, nadzakufikitsa kwa Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Akanani, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndidzawaononga.

24 Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kucita monga mwa nchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao.

25 Ndipo muzitumikira Yehova Mulungu wanu, potero adzadalitsa cakudya cako, ndi madzi ako; ndipo ndidzacotsa nthenda pakati pa iwe.

26 M'dziko mwanu simudzakhala wakutaya mwana, kapena wosabala; ndidzakwaniritsa kuwerenga kwa masiku ako.

27 Ndidzatumiza kuopsa kwanga kukutsogolere, ndipo ndidzapitikitsa anthu onse amene udzafika kwao, ndipo ndidzacita kuti adani ako onse adzakuonetsa m'mbuyo mwao.

28 Ndipo ndidzatumiza mabvu akutsogolere amene adzaingitsa Ahivi, Akanani, ndi Ahiti, pamaso pako.

29 Sindidzawaingista pamaso pako caka cimodzi; kuti dziko lingakhale bwinja, ndi zirombo za kuthengo zingakucurukire.

30 Ndidzawaingitsa pang'ono pang'ono pamaso pako, kufikira utacuruka, ndi kulandira dziko colowa cako.

31 Ndipo ndidzalemba malire ako kuyambira ku Nyanja Yofiira, kufikira ku nyanja ya Afilisiti, ndi kuyambira kucipululu kufikira ku Nyanja; popeza ndidzapereka okhala m'dzikolo m'dzanja lako, ndipo uziwaingitsa pamaso pako.

32 Usapangana nao, kapena ndi milungu yao.

33 Asakhale m'dziko lako iwowa, kuti angakulakwitse pa loe; pakuti ukatumikira milungu yao, kudzakukhalira msampha ndithu.