3 Isakara, Zebuloni, ndi Benjamini;
4 Dani ndi Nafitali, Gadi ndi Aseri.
5 Ndipo amoyo onse amene anaturuka m'cuunomwace mwa Yakobo ndiwo makumi asanu ndi awiri; kama Yosefe anali m'Aigupto.
6 Ndipo anafa Yosefe, ndi abale ace onse, ndi mbadwo uwo wonse.
7 Ana a Israyeli ndipo anaswana, nabalana, nacuruka, nakhala nazo mphamvu zazikuru; ndipo dziko linadzala nao.
8 Pamenepo inalowa mfumu yatsopano m'ufumu wa Aigupto, imene siinadziwa Yosefe.
9 Ndipo ananena ndi anthu ace, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israyeli, acuruka, natiposa mphamvu.