3 Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzicepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;
4 pakuti ukakana kulola anthu anga amuke, taona, mawa ndidzafikitsa dzombe m'dziko lako;
5 ndipo lidzakuta nkhope ya dziko, kotero, kuti palibe munthu adzakhoza kuona dziko; ndipo lidzadya zotsalira zidapulumuka, zidatsalira inu pamatalala, ndipo lidzadya mtengo uti wonse wokuphukirani kuthengo;
6 ndipo lidzadzaza m'nyumba zako, ndi m'nyumba za anyamata ako onse, ndi m'nyumba za Aaigupto onse; sanaciona cotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo pa dziko lapansi kufikira lero lino. Ndipo anatembenuka, naturuka kwa Farao.
7 Ndipo anyamata ace a Farao ananena naye, Ameneyo amaticitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wao. Kodi simunayambe kudziwa kuti Aigupto laonongeka?
8 Ndipo anawabwereretsa Mose ndi Aroni kwa Farao, nanena nao, Mukani, katumikireni Yehova Mulungu wanu. Koma amene adzapitawo ndiwo ani?
9 Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akuru athu, ndi ana athu amuna ndi akazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu; pakuti tiri nao madyerero a Yehova.