2 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga,Ndipo wakhala cipulumutso canga;Ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza:Ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzammveketsa.
3 Yehova ndiye wankhondo;Dzina lace ndiye Yehova.
4 Magareta a Farao ndi nkhondo yace anawaponya m'nyanja;Ndi akazembe ace osankhika anamira m'Nyanja Yofiira.
5 Nyanja inawamiza:Anamira mozama ngati mwala.
6 Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu,Dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani.
7 Ndipo ndi ukulu wanu waukuru mwapasula akuukira Inu;Mwatumiza mkwiyo wanu, unawanyeketsa ngati ciputu.
8 Ndipondi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika,Mayendedwe ace anakhala ciriri ngati mulu;Zozama zinalimba m'kati mwa nyanja.