11 Ndipo kunakhala, pamene Mose anakweza dzanja lace Israyeli analakika; koma pamene anatsitsa dzanja lace Amaleki analakika.
12 Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ace, wina mbali yina, wina mbali yina; ndi manja ace analimbika kufikira litalowa dzuwa.
13 Ndipo Yoswa anatyola Amaleki ndi anthu ace ndi kuukali kwa lupanga.
14 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ici m'buku, cikhale cikumbutso, nucimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse cikumbukilo ca Amaleki pansi pa thambo.
15 Ndipo Mose anamanga guwa la nsembe, nalicha dzina lace Yehova Nisi:
16 nati, Yehova walumbira: padzakhala nkhondo ya Yehova pa Amaleki m'mibadwo mibadwo.