5 Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusunga cipangano canga, ndidzakuyesani cuma canga ca padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa;
6 ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a lsrayeli.
7 Ndipo Mose anadza, naitana akuru a anthu, nawaikira pamaso pao mau awa onse amene Yehova adamuuza.
8 Ndipo anthu onse anabvomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazicita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.
9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akubvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo.
10 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zobvala zao,
11 nakonzekeretu tsiku lacitatu; pakuti tsiku lacitatu Yehova adzatsika pa phiri la Sinai pamaso pa anthu onse.