23 Koma ngati kuphweteka kukalipo, uzipereka moyo kulipa moyo,
24 diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi,
25 kutentha kulipa kutentha, bala kulipa bala, mkwapulo kulipa mkwapulo.
26 Munthu akampanda mnyamata wace, kapena mdzakazi wace, padiso, nalithudzula, azimlola amuke waufulu cifukwa ca diso lace.
27 Ndipo akagurula dzino la mnyamata wace, kapena dzino la mdzakazi wace, azimlola amuke waufulu cifukwa ca dzino lace.
28 Ng'ombe ikatunga mwamuna kapena mkazi, nafa, aiponyetu miyala ng'ombeyo, osadya nyama yace; koma mwini ng'ombeyo azimasuka.
29 Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamcenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini waceyo amuphenso.