1 Munthu akaba ng'ombe, kapena nkhosa, nakaipha, kapena kuigulitsa, azilipa ng'ombe zisanu pa ng'ombeyo; ndi nkhosa zinai pa nkhosayo,
2 Akampeza wakuba alimkuboola, nakamkantha kotero kuti wafa, palibe camwazi.
3 Litamturukira dzuwa, pali camwazi; wakubayo azilipa ndithu; ngati alibe kanthu, amgulitse pa umbala wace.
4 Akacipeza cakubaco ciri m'dzanja lace camoyo, ngakhale ng'ombe, kapena buru, kapena nkhosa, alipe mowirikiza.
5 Munthu akadyetsa coweta pabusa kapena pa munda wamphesa, atamasula coweta cace, ndipo citadya podyetsa pa mwini wace; alipe podyetsa pace poposa, ndi munda wa mphesa wace woposa.