1 Ndipo iye ananena ndi Mose, Ukwere kudza kwa Yehova, iwe ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akuru a Israyeli makumi asanu ndi awiri; ndipo mugwadire pakudza kutali;
2 ndipo Mose yekha ayandikire kwa Yehova; koma asayandikire iwowa; ndi anthunso asakwere naye.
3 Ndipo Mose anadza nafotokozera anthu mau onse a Yehova, ndi masveruzo onse; ndipo anthu onse anabvomera pamodzi, nati, Mau onse walankhula Yehova tidzacita.
4 Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde pa phiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.
5 Ndipo anatuma ana a Israyeli a misinkhu ya anyamata, ndiwo anapereka nsembe zopsereza, naphera Yehova nsembe zamtendere, zang'ombe.
6 Ndipo Mose anagawa mwaziwo, nathira wina m'zotengera, nawaza wina pa guwa la nsembe.