4 Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde pa phiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.
5 Ndipo anatuma ana a Israyeli a misinkhu ya anyamata, ndiwo anapereka nsembe zopsereza, naphera Yehova nsembe zamtendere, zang'ombe.
6 Ndipo Mose anagawa mwaziwo, nathira wina m'zotengera, nawaza wina pa guwa la nsembe.
7 Ndipo anatenga buku la Cipangano, nawerenga m'makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzacita, ndi kumvera.
8 Ndipo Mose anatenga mwaziwo, nawaza pa anthu, nati, Taonani mwazi wa cipangano, cimene Yehova anacita nanu, kunena za mau awa onse,
9 Ndipo Mose ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akuru a Israyeli makumi asanu ndi awiri anakwerako;
10 ndipo anapenya Mulungu wa Israyeli; ndipo pansi pa mapazi ace panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiri, ndi ngati thupi la thambo loti mbe.