3 Ndipo uzipanga zotayira zace zakulandira mapulusa ace, ndi zoolera zace, ndi mbale zowazira zace, ndi mitungo yace, ndi zoparira moto zace; zipangizo zace zonse uzipanga zamkuwa.
4 Ndipo ulipangire made, malukidwe ace ndi amkuwa; nupange pa malukidwewo ngondya zace zinai mphete zinai zamkuwa.
5 Nuwaike pansi pa matso a guwa la nsembelo posungulira, kuti malukidwe alekeze pakati pa guwa la nsembelo.
6 Ndipo upangire guwa la nsembe mphiko, mphiko za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi mkuwa.
7 Ndipo apise mphiko m'mphetezo kuti mphikozo zikhale pa mbali ziwiri za guwa la nsembe polinyamula.
8 Ulipange lagweregwere ndi matabwa; monga anakuonetsa m'phirimo; alipange momwemo.
9 Upangenso bwalo la cihema; pa mbali yace ya kumwela, kumwela, pakhale nsaru zocingira zakubwaloza nsaru ya bafuta wa thonje losansitsa, utali wace wa pa mbali imodzi mikono zana;