3 Ndipou lankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zobvala apatulidwe nazo, andicitire Ine nchito ya nsembe.
4 Ndipo zobvala azisoka ndizi: capacifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ace zobvala zopatulika, kuti andicitire Ine nchito ya nsembe,
5 Ndipo atenge golidi, ndi lamadzi ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
6 Naombe efodi ndi golidi, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya mmisiri.
7 Akhale nazo zapamapewa ziwiri zomangika ku nsonga zace ziwiri, kuti amangike nazo.
8 Ndipo mpango wa efodi, wokhala pamenepo, kuti ammange nao, ukhale wa ciombedwe comweco, ndi woombera kumodzi, wagolidi, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
9 Ndipo utenge miyala iwiri yaberulo, nulocepo maina a ana a Israyeli;