15 Utengenso nkhosa yamphongo imodziyo; ndi Aroni ndi ana ace amuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.
16 Nuiphe nkhosa yamphongoyo, ndi kutenga mwazi wace, ndi kuuwaza pa guwa la nsembe pozungulira.
17 Ndipo upadzule nkhosa yamphongo m'ziwalo zace, ndi kutsuka matumbo ace, ndi miyendo yace, ndi kuziika pa ziwalo zace, ndi pamutu pace.
18 Pamenepo upsereze, nkhosa yamphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza ya Yehova, ya pfungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.
19 Ndipo utenge nkhosa yamphongo yinayo; ndi Aroni ndi ana ace amuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.
20 Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wace, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja la ana ace amuna, ndi pa cala cacikulu ca dzanja lao lamanja, ndi pa cala cacikulu ca phazi lao lamanja, ndi kuuwaza mwaziwo pa guwa la nsembe posungulira,
21 Ndipo utapeko pamwazi uli pa guwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zobvala zace, ndi pa ana ace amuna, ndi pa zobvala za ana ace amuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zobvala zace zomwe, ndi ana ace amuna ndi zobvala zao zomwe pamodzi ndi iye.