5 Pamenepo utenge zobvalazo ndi kubveka Aroni maraya am'kati, ndi mwinjiro wa efodi, ndi efodi, ndi capacifuwa, ndi kummangira m'cuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru;
6 ndipo uike nduwira pamutu pace, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo.
7 Pamenepo utenge mafuta odzoza nao nuwatsanulire pamutu pace, ndi kumdzoza.
8 Ndipo ubwere nao ana ace amuna ndi kuwabveka maraya am'kati.
9 Uwamangirenso Aroni ndi ana ace amuna mipango m'cuuno mwao, nuwamangire akapa pamutu pao; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; nudzaze dzanja la Aroni ndi dzanja la ana ace amuna,
10 Ndipo ubwere nayo ng'ombe yamphongo patsogolo pa cihema cokomanako; ndipo Aroni ndi ana ace amuna aike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo.
11 Nuphe ng'ombe yamphongoyo pamaso pa Yehova, pa khomo la cihema cokomanako.