1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, kwera kucokera kuno, iwe ndi anthu amene unawakweza kucokera m'dziko la Aigupto, kumka ku dzikolo ndinalumbirira nalo Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzapatsa mbeu zako ilo;
2 ndipo ndidzatuma mthenga akutsogolere; ndipo ndidzapitikitsa Akanani, ndi Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;
3 kudziko koyenda mkaka ndi uci ngati madzi; pakuti sindidzakwera pakati pa inu; popeza inu ndinu anthu opulupudza; ndingathe inu panjira.
4 Ndipo pamene anthu anamva mau awa oipa anacita cisoni; ndipo panalibe mmodzi anabvala zokometsera zace.
5 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi ana a Israyeli, Inu ndinu anthu opulupudza; ndikakwera kulowa pakati pa inu kamphindi kamadzi, ndidzakuthani; koma tsopano, bvulani zokometsera zanu, kuti ndidziwe comwe ndikucitireni.
6 Ndipo ana a Israyeli anazicotsera zokometsera zao kuyambira pa phiri la Horebe.
7 Ndipo Mose akatenga cihemaco nacimanga kunja kwa cigono, kutari kwa cigono; nacicha, Cihema cokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anaturuka kumka ku cihema cokomanako kunja kwa cigono.