5 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi ana a Israyeli, Inu ndinu anthu opulupudza; ndikakwera kulowa pakati pa inu kamphindi kamadzi, ndidzakuthani; koma tsopano, bvulani zokometsera zanu, kuti ndidziwe comwe ndikucitireni.
6 Ndipo ana a Israyeli anazicotsera zokometsera zao kuyambira pa phiri la Horebe.
7 Ndipo Mose akatenga cihemaco nacimanga kunja kwa cigono, kutari kwa cigono; nacicha, Cihema cokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anaturuka kumka ku cihema cokomanako kunja kwa cigono.
8 Ndipo kunali, pakuturuka Mose kumka ku cihemaco kuti anthu onse anaimirira, nakhala ciriri, munthu yense pakhomo pa hema wace, nacita cidwi pa Mose, kufikira atalowa m'cihemaco.
9 Ndipo kunali, pakulowa Mose m'cihemaco, mtambo njo udafutsika, nuima pakhomo pa cihemaco; ndipo Yehova analankhula ndi Mose.
10 Ndipo anthu onse anaona mtambo njo ulikuima pakhomo pa cihema; ndi anthu onse anaimirira, nalambira, yense pakhomo pa hema wace.
11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lace. Ndipo anabwerera kumka kucigono; koma mtumiki wace Yoswa, mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wace, sanacoka m'cihemamo.