1 Ndipo Bezaleli anapanga likasa la mtengo wasitimu; utali wace mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwace mkono ndi hafu, ndi msinkhu wace mkono ndi hafu;
2 ndipo analikuta ndi golidi woona m'kati ndi kunja, nalipangira mkombero wagolidi pozungulira pace.
3 Ndipo analiyengera mphete zinai zagolidi pa miyendo yace inai; mphete ziwiri pa mbali yace imodzi, ndi mphete: ziwiri pa mbali yace yina.
4 Ndipo anapanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndi golidi.
5 Ndipo anapisa mphiko m'mphetezo pa mbali zace za likasalo, kuti anyamulire nazo likasa.
6 Ndipo anapanga cotetezerapo ca golidi woona; utali wace mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwace mkono ndi hafu.