27 nafukizapo cofukiza ca pfungo lokoma; monga Yehova adamuuza Mose.
28 Ndipo anapacika kukacisi nsaru yotsekera pakhomo.
29 Ndipo anaika guwa la nsembe yopsereza pa khomo la kacisi wa cihema cokomanako, natenthapo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa; monga Yehova adamuuza Mose.
30 Ndipo anaika mkhate pakati pa cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe; nathiramo madzi osamba.
31 Ndipo Mose ndi Aroni ndi ana ace amuna anasamba manja ao ndi mapazi ao m'menemo;
32 pakulowa iwo m'cihema cokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose.
33 Ndipo anautsa mpanda pozungulira pa cihema ndi guwa la nsembe, napacika nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo. Momwemo Mose anatsiriza nchitoyi.