33 Ndipo anautsa mpanda pozungulira pa cihema ndi guwa la nsembe, napacika nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo. Momwemo Mose anatsiriza nchitoyi.
34 Pamenepo mtambo unaphimba cihema cokomanako, ndi ulemerero wa Yehova unadzaza kacisiyo.
35 Ndipo Mose sanathe kulowa m'cihema cokomanako, popeza mtambo unakhalabe pamenepo; ndi ulemerero wa Yehova unadzaza kacisi.
36 Ndipo pakukwera mtambo kucokera kukacisi, ana a Israyeli amayenda maulendo ao onse;
37 koma ukapanda kukwera mtambo, samayenda ulendo wao kufikira tsiku loti wakwera.
38 Pakuti mtambo wa Yehova unakhala pakacisi msana, ndi usiku munali moto m'menemo, pamaso pa mbumba yonse ya Israyeli, m'maulendo ao onse.