1 Ndipo pambuyo pace Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Lola anthu anga apite, kundicitira madyerero m'cipululu.
2 Koma Farao anati, Yehova ndani, kuti ndimvere mau ace ndi kulola Israyeli apite? Sindimdziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israyeli apite.
3 Ndipo iwo anati, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; timuketu ulendo wa masiku atatu m'cipululu, kumphera nsembe Yehova Mulungu wathu; kuti angatikumike ndi mliri, kapena ndi lupanga,
4 Ndipo mfumu ya Aigupto inanena nao, Inu, Mose ndi Aroni, cifukwa ninji mumasulira anthu nchito zao? Mukani ku akatundu anu.
5 Farao anatinso, Taonani, anthu a m'dziko ndiwo ambiri tsopano; ndipo inu muwapumitsa ku akatundu ao,
6 Ndipo tsiku lomwelo Farao analamulira akufulumiza anthu, ndi akapitao ao, ndi kuti,