6 Ndipo tsiku lomwelo Farao analamulira akufulumiza anthu, ndi akapitao ao, ndi kuti,
7 Musawapatsanso anthu udzu wakupanga nao njerwa monga kale; apite okha adzifunire udzu.
8 Ndipo muziwawerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musacepsapo, popeza acita cilezi; cifukwa cace alikupfuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu.
9 Ilimbike nchito pa amunawo, kuti aigwiritsitse, asasamalire mau amabodza.
10 Ndipo akufulumiza anthu ndi akapitao ao anaturuka, nanena ndi anthu ndi kuti, Atero Farao, Kulibe kukupatsani udzu.
11 Mukani inu nokha, dzifunireni udzu komwe muupeza; pakuti palibe kanthu kadzacepa pa nchito yanu.
12 Pamenepo anthuwo anabalalika m'dziko lonse la Aigupto kufuna ciputu ngati udzu.