2 Ndipo Mulungu ananena ndi Mose, nati kwa iye, Ine ndine YEHOV A:
3 ndipo ndinaonekera Abrahamu, Isake ndi Yakobo, Mulungu Wamphamvuyonse; koma sindinadziwika kwa iwo ndi dzina langa YEHOV A.
4 Ndipo ndinakhazikitsanso nao cipangano canga, kuwapatsa dziko la Kanani, dziko la maulendo ao, anali alendo m'mwemo.
5 Ndamvanso kubuula kwa ana a Israyeli, amene Aaigupto awayesa akapolo; ndipo ndakumbukila cipangano canga.
6 Cifukwa cace nena kwa ana a Israyeli, Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakuturutsani pansi pa akatundu a Aaigupto, ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo akuru;
7 ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakuturutsa inu pansi pa akatundu a Aaigupto.
8 Ndipo ndidzakulowetsani m'dziko limene ndinakweza dzanja langa kunena za ilo, kuti ndilipereke kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo; ndipo ndidzakupatsani ilo likhale lanulanu; Ine ndine Yehova.