25 Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana akazi a Putieli akhale mkazi wace, ndipo anambalira Pinehasi. Amenewo ndi akuru a makolo a Alevi mwa mabanja ao.
26 Omwewo ndiwo Aroni ndi Mose amene Yehova ananena nao, Turutsani ana a Israyeli m'dziko la Aigupto mwa makamu ao.
27 Awa ndi omwewo ananena ndi Farao, mfumu ya Aigupto, awaturutse ana a Israyeli m'Aigupto; Mose ndi Aroni amenewa.
28 Ndipo kunali, tsiku limene Yehova ananena ndi Mose m'dziko la Aigupto,
29 Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Ine ndine Yehova: lankhula ndi Farao mfumu ya Aigupto zonsezi Ine ndizinena nawe.
30 Koma Mose anati pamaso pa Yehova, Onani, ine ndiri wa milome yosadula, ndipo Farao adzandimvera bwanji?