3 Koma Ine ndidzaumitsa mtima wace wa Farao, ndipo ndidzacurukitsa zizindikilo ndi zozizwa zanga m'dziko la Aigupto.
4 Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aigupto, ndipo ndidzaturutsa makamu anga, anthu anga ana a Israyeli, m'dziko la Aigupto ndi maweruzo akuru.
5 Ndipo Aaigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakutambasula Ine dzanja langa pa Aigupto, ndi kuturutsa ana a Israyeli pakati pao.
6 Ndipo Mose ndi Aroni anacita monga Yehova anawalamulira, momwemo anacita.
7 Ndipo Mose anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu, ndi Aroni anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu kudza zitatu, pamene ananena ndi Farao.
8 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, ndi kuti,
9 Pamene Farao adzalankhula nanu, ndi kuti, Dzicitireni codabwiza; pamenepo uzinena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, Iponye pansi pamaso pa Farao, isanduke cinjoka,