7 Ndipo Mose anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu, ndi Aroni anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu kudza zitatu, pamene ananena ndi Farao.
8 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, ndi kuti,
9 Pamene Farao adzalankhula nanu, ndi kuti, Dzicitireni codabwiza; pamenepo uzinena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, Iponye pansi pamaso pa Farao, isanduke cinjoka,
10 Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao, nacita monga momwe Yehova adawalamulira; ndipo Aroni anaponya pansi ndodo yace pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ace, ndipo inasanduka cinjoka,
11 Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aigupto, iwonso anacita momwemo ndi matsenga ao.
12 Pakuti yense anaponya pansi ndodo yace, ndipo zinasanduka zinjoka; koma ndodoya Aroni inameza ndodo zao,
13 Koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvera iwo; monga adalankhula Yehova.