12 Pamenepo anabwera ku Yerusalemu kucokera ku phiri lonenedwa la Azitona, limene liyandikana ndi Yerusalemu, loyendako tsiku la Sabata.
13 Ndipo pamene adalowa, anakwera ku cipinda ca pamwamba, kumene analikukhalako; ndiwo Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi Andreya, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeyu ndi Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyu, ndi Simoni Zelote, ndi Yuda mwana wa Yakobo.
14 Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Mariya, amace wa Yesu, ndi abale ace omwe.
15 Ndipo m'masiku awa anaimirira Petro pakati pa abale, nati (gulu la anthu losonkhana pamalo pomwe ndilo ngati zana limodzi ndi makumi awiri),
16 Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m'kamwa mwa Davine za Yudase, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.
17 Cifukwa anali wowerengedwa mwa ife, ndipo analandira gawo lace la utumiki uwu.
18 (Uyutu tsono anadzitengera kadziko ndi mphoto ya cosalungama; ndipo anagwa camutu, naphulika pakati, ndi matumbo ace onse anakhuthuka;