3 Kunacitika tsono, utamkhazikikira ufumu, anapha anyamata ace amene adapha mfumu atate wace.
4 Koma sanapha ana ao, koma anacita monga umo mulembedwa m'cilamulo, m'buku la Mose, monga Yehova analamulira, ndi kuti, Atate asafere ana, ndi ana asafere atate; koma yense afere chimo lace lace.
5 Ndipo Amaziya anamemeza Ayuda, nawaika monga mwa nyumba za atate ao, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo onse a Yuda ndi Benjamini; nawawerenga a zaka makumi awiri ndi mphambu, nawapeza amuna osankhika zikwi mazana atatu akuturukira kunkhondo, ogwira mkondo ndi cikopa.
6 Analemberanso ngwazi zamphamvu za m'Israyeli zikwi zana limodzi, kuwalipira matalente a siliva zana limodzi.
7 Koma anamdzera munthu wa Mulungu, kuti, Mfumu, khamu la nkhondo la Israyeli lisapite nanu; pakuti Yehova sakhala ndi Israyeli, sakhala ndi ana onse a Efraimu.
8 Koma ngati mumuka, citani, limbikani kunkhondo, Mulungu adzakugwetsani pamaso pa adani; pakuti Mulungu ali nayo mphamvu yakuthandiza ndi yakugwetsa.
9 Ndipo Amaziya anati kwa munthu wa Mulungu, Koma nanga titani nao matalente zana limodzi ndinapatsa ankhondo a Israyeli? Nati munthu wa Mulungu, Yehova ali nazo zoposa izi kukupatsani.