19 Nanenera Mulungu wa Yerusalemu, monga umo amanenera milungu ya mitundu ya anthu a pa dziko lapansi, ndiyo nchito ya manja a anthu.
20 Ndipo Hezekiya mfumu, ndi Yesaya mneneri mwana wa Amozi, anapemphera pa ici, napfuulira Kumwamba.
21 Ndipo Yehova anatuma wamthenga amene anaononga ngwazi zamphamvu zonse, ndi atsogoleri, ndi akazembe, ku cigono ca mfumu ya Asuri. Nabwerera iye ndi nkhope yamanyazi ku dziko lace. Ndipo atalowa m'nyumba ya mulungu wace, iwo oturuka m'matumbo mwace anamupha ndi lupanga pomwepo.
22 Momwemo Yehova analanditsa Hezekiya ndi okhala m'Yerusalemu m'dzanja la Sanakeribu mfumu ya Asuri, ndi m'dzanja la onse ena, nawatsogolera monsemo.
23 Ndipo ambiri anabwera nayo mitulo kwa Yehova ku Yerusalemu, ndi za mtengo wace, kwa Hezekiya mfumu ya Yuda; nakwezeka iye pamaso pa amitundu onse kuyambira pomwepo.
24 Masiku omwe aja Hezekiya anadwala pafupi imfa; ndipo anapemphera kwa Yehova; ndi Iye ananena naye, nampatsa cizindikilo codabwiza.
25 Koma Hezekiya sanabwezera monga mwa cokoma anamcitira, pakuti mtima wace unakwezeka; cifukwa cace unamdzera mkwiyo iye, ndi Yuda, ndi Yerusalemu.