24 Masiku omwe aja Hezekiya anadwala pafupi imfa; ndipo anapemphera kwa Yehova; ndi Iye ananena naye, nampatsa cizindikilo codabwiza.
25 Koma Hezekiya sanabwezera monga mwa cokoma anamcitira, pakuti mtima wace unakwezeka; cifukwa cace unamdzera mkwiyo iye, ndi Yuda, ndi Yerusalemu.
26 Koma Hezekiya anadzicepetsa m'kudzikuza kwa mtima wace, iye ndi okhala m'Yerusalemu, momwemo mkwiyo wa Yehova sunawadzera masiku a Hezekiya.
27 Ndipo cuma ndi ulemu zinacurukira Hezekiya, nadzimangira iye zosungiramo siliva, ndi golidi, ndi timiyala ta mtengo wace, ndi zonunkhira, ndi zikopa, ndi zipangizo zokoma ziri zonse;
28 ndi nyumba zosungiramo zipatso za tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zipinda za nyama iri yonse, ndi makola a zoweta.
29 Nadzimangiranso midzi, nadzionera nkhosa ndi ng'ombe zocuruka; pakuti Mulungu adampatsa cuma cambirimbiri.
30 Hezekiya yemweyo anatseka kasupe wa kumtunda wa madzi a Gihoni, nawapambutsa atsikire ku madzulo kwa mudzi wa Davide. Ndipo Hezekiya analemerera nazo nchito zace zonse.