9 Koma Manase analakwitsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu, kotero kuti anacita coipa koposa amitundu, amene Yehova anawaononga pamaso pa ana a Israyeli.
10 Ndipo Yehova analankhula ndi Manase ndi anthu ace, koma sanasamalira.
11 Motero Yehova anawafikitsira akazembe a khamu la nkhondo la mfumu ya Asuri, namgwira Manase ndi zokowera, nammanga matangadza, namuka naye ku Babulo.
12 Ndipo popsinjika iye anapembedza Yehova Mulungu wace, nadzicepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ace.
13 Anampempha, ndipo anapembedzeka, namvera kupembedza kwace, nambwezera ku Yerusalemu m'ufumu wace. Pamenepo anadziwa Manase kuti Yehova ndiye Mulungu.
14 Citatha ici tsono iye anaumangira mudzi wa Davide linga lakunja, kumadzulo kwa Gihoni, m'cigwa, mpaka polowera pa cipata cansomba; nazinga Ofeli, nalikweza kwambiri; anaikanso akazembe a nkhondo m'midzi yonse yamalinga ya m'Yuda.
15 Ndipo anacotsa milungu yacilendo, ndi fanoli m'nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse a nsembe anawamanga m'phiri la nyumba ya Yehova ndi m'Yerusalemu, nawataya kunja kwa mudzi.