1 Pamenepo Yosiya anacitira Yehova Paskha m'Yerusalemu, naphera Paskha tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi woyamba.
2 Ndipo anaika ansembe pa udikiro wao, nawalimbikitsa acite utumiki wa nyumba ya Yehova.
3 Nati kwa Alevi akuphunzitsa Aisrayeli onse, ndiwo opatulima Yehova, Ikani likasa lopatulika m'nyumba imene Solomo mwana wa Davide mfumu ya Israyeli anaimanga; silikhalanso katundu pa mapewa anu; tsopano mutumikire Yehova Mulungu wanu, ndi anthu ace Israyeli.
4 Ndipo mudzikonzere monga mwa nyumba za makolo anu, m'zigawo zanu, monga umo adalembera Davide mfumu ya Israyeli, ndi umo adalembera Solomo mwana wace.
5 Ndipo muimirire m'malo opatulika, monga mwa magawidwe a nyumba za makolo za abale anu ana a anthu, akhale nalo onse gawo la nyumba ya makolo ya Alevi.
6 Ndipo muphere Paskha, nimudzipatule ndi kukonzera abale anu, kucita monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.