8 Ndi akulu ace anapatsa nsembe yaufulu kwa anthu, kwa ansembe, ndi kwa Alevi. Hilikiya ndi Zekariya ndi Yehieli, atsogoleri a m'nyumba ya Mulungu, anapatsa ansembe zoweta zazing'ono zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi, ndi ng'ombe mazana atatu, zikhale nsembe za Paskha.
9 Konaniyanso, ndi Semaya, ndi Netaneli, abale ace, ndi Hasabiya, ndi Yeyeli, ndi Yosabadi, akuru a Alevi, ana patsa Alevi zoweta zazing'ono zikwi zisanu, ndi ng'ombe mazana asanu, zikhale nsembe za Paskha.
10 Momwemo anakonzera kutumikiraku, naima ansembe pokhala pao, ndi Alevi m'zigawo zao, monga umo adawauzira mfumu.
11 Pamenepo anaphera Paskha; ndi ansembe anawaza mwazi adaulandira m'manja mwa Alevi amene anasenda nsembezo.
12 Ndipo anacotsapo nsembe zopsereza, kuti azipereke kwa ana a anthu monga mwa magawidwe a nyumba za makolo; azipereke kwa Yehova monga mulembedwa m'buku la Mose. Natero momwemo ndi ng'ombezo.
13 Ndipo anaoca Paskha pamoto, monga mwa ciweruzo; koma zopatulikazo anaziphika m'miphika, ndi m'mitsuko, ndi m'ziwaya; nazipereka msanga kwa ana onse a anthu.
14 Ndi pambuyo pace anadzikonzera okha ndi ansembe; popeza ansembe, ana a Aroni, analikupereka nsembe zopsereza ndi mafuta mpaka usiku; cifukwa cace Alevi anadzikonzera okha ndi ansembe ana a Aroni.