6 ndi Balati, ndi midzi yonse yosungiramo cuma anali nayo Solomo, ndi midzi yonse ya magareta ace, ndi midzi ya apakavalo ace, ndi zonse anazifuna Solomo kuzimanga zomkondweretsa m'Yerusalemu, ndi m'Lebano, ndi m'dziko lonse la ufumu wace.
7 Ndipo anthu onse otsala mwa Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, osati Aisrayeli,
8 mwa ana ao otsala m'dziko pambuyo pao, amene ana a Israyeli sanawatha, mwa iwowa Solomo anawacititsa thangata mpaka lero lino.
9 Koma mwa ana a Israyeli Solomo sanawayesa akapolo omgwirira nchito; koma iwowa anali anthu a nkhondo, akazembe ace akuru, ndi akuru a magareta ace, ndi apakavalo ace.
10 Amenewa anali akuru a akapitao a mfumu Solomo, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu akulamulira anthu.
11 Ndipo Solomo anamkweretsa mwana wamkazi wa Farao m'mudzi wa Davide, alowe m'nyumba imene adammangira; pakuti anati, Mkazi wanga asakhale m'nyumba ya Davide mfumu ya Israyeli; popeza mpopatulika pamene panafika likasa la Yehova.
12 Pamenepo Solomo anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa la nsembe la Yehova, limene adalimanga pakhomo palikole,