1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao; pakuti ndaumitsa mtima wace, ndi mtima wa anyamata ace, kuti ndiike zizindikilo zanga izi pakati pao;
2 ndi kuti ufotokozere, m'makutu a ana ako, ndi a zidzukulu zako, comwe ndidzacita m'Aigupto, ndi zizindikilo zanga zimene ndinaziika pakati pao; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.
3 Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzicepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;
4 pakuti ukakana kulola anthu anga amuke, taona, mawa ndidzafikitsa dzombe m'dziko lako;