17 Ndipo tsopano, ndikhululukirenitu kulakwa kwanga nthawi yino yokha, nimundipembere kwa Yehova Mulungu wanu, kuti andicotsere imfa yino yokha.
18 Ndipo anaturuka kwa Farao, napemba Yehova.
19 Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya m'Nyanja Yofiira: silinatsala dzombe limodzi pakati pa malire onse a Aigupto.
20 Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, ndipo sanalola ana a Israyeli amuke.
21 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kuthambo, ndipo padzakhala mdima pa dziko la Aigupto, ndiwo mdima wokhudzika.
22 Ndipo Mose anatambasulira dzanja lace kuthambo; ndipo munali mdima bii m'dziko lonse la Aigupto masiku atatu;
23 sanaonana, sanaukanso munthu pamalo pace, masiku atatu; koma kwa ana onse a Israyeli kudayera m'nyumba zao.