24 Ndipo anthu anadandaulira Mose, ndi kuti, Tidzamwa ciani?
25 Ndipo iye anapfuulira kwa Yehova; ndipo Yehova anamsonyeza mtengo ndipo anauponya m'madzimo, ndi madzi anasanduka okoma. Pamenepo anawapangira lemba ndi ciweruzo, ndi pomwepa anawayesa;
26 ndipo anati, Ngati udzamveratu mau a Yehova, Mulungu wako, ndi kucita zoona pamaso pace, ndi kuchera khutu pa malamulo ace, ndi kusunga malemba ace onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aaigupto sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti Ine Yehova ndine wakuciritsa iwe.
27 Ndipo anafika pa Elimu, ndi pamenepo panali akasupe a madzi khumi ndi awiri, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; ndipo anamanga cigono cao pomwepo pa madziwo.