1 Ndipo anacoka ku Elimu, ndi khamu lonse la ana a Israyeli linalowa m'cipululu ca Sini, ndico pakati pa Elimu ndi Sinai, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi waciwiri ataturuka m'dziko la Aigupto.
2 Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli linadandaulira Mose ndi Aroni m'cipululu;
3 nanena nao ana a Israyeli, Ha! mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Aigupto, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife cokhuta; pakuti mwatiturutsa kudza nafe m'cipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.
4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndidzabvumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituruka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lace, kuti ndiwayese, ngati ayenda m'cilamulo canga kapena iai.