15 Ndipo pamene ana a Israyeli anakaona, anati wina ndi mnzace, Nciani ici? pakuti sanadziwa ngati nciani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale cakudya canu,
16 Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yace; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m'hema mwace.
17 Ndipo ana a Israyeli anatero, naola wina wambiri, wina pang'ono.
18 Ndipo pamene anayesa ndi omeri, iye amene adaola wambiri sunamtsalira, ndi iye amene adaola pang'ono sunamsowa; yense anaola monga mwa njala yace.
19 Ndipo Mose ananena nao, Palibe munthu asiyeko kufikira m'mawa.
20 Koma sanammvera Mose; ndipo ena anasiyako kufikira m'mawa; koma unagwa mphutsi, nununkha. Ndipo Mose anakwiya nao.
21 Ndipo anauola m'mawa ndi m'mawa, yense monga mwa njala yace; popeza likatentha dzuwa umasungunuka.