20 Koma sanammvera Mose; ndipo ena anasiyako kufikira m'mawa; koma unagwa mphutsi, nununkha. Ndipo Mose anakwiya nao.
21 Ndipo anauola m'mawa ndi m'mawa, yense monga mwa njala yace; popeza likatentha dzuwa umasungunuka.
22 Ndipo kunali tsiku lacisanu ndi cimodzi, anaola mkate, naonjezapo linzace, maomeri awiri pa munthu mmodzi; ndipo akazembe a khamulo anadza nauza Mose.
23 Ndipo ananena nao, Ici ndi comwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; cimene muzioca, ocani, ndi cimene muziphika phikani; ndi cotsala cikukhalireni cosunguka kufikira m'mawa.
24 Ndipo anausunga kufikira m'mawa, monga adalamulira Mose; koma sunanunkha, ndipo sunagwa mphutsi.
25 Ndipo Mose anati, Muudye lero; pakuti lero ndilo Sabata la Yehova; simuupeza lero pabwalo.
26 Muziola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lacisanu ndi ciwiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe.