8 Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife ciani? simulikudandaulira ife koma Yehova.
9 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Nena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, Yandikizani pamaso pa Yehova, pakuti anamva madandaulo anu.
10 Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israyeli kuti iwo anatembenukira kucipululu, ndipo, taonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo.
11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
12 Ndamva madandaulo a ana a Israyeli; lankhula nao ndi kuti, Madzulo mudzadya nyama, ndi m'mawa mudzakhuta mkate; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
13 Ndipo kunali madzulo zinakwera zinziri, ndipo zinakuta tsasa, ndi m'mawa padagwa mame pozungulira tsasa.
14 Ndipo atasansuka mame adagwawo, taonani, pankhope pa cipululu pali kanthu kakang'ono kamphumphu, kakang'ono ngati cipale panthaka.