1 Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli linacoka m'cipululu ca Sini, m'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona m'Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.
2 Pamenepo anthu anatsutsana ndi Mose, nati, Tipatseni madzi timwe, Koma Mose ananena nao, Mutsutsana nane bwanji? Muyeseranji Yehova?
3 Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kucokera ku Aigupto, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu?
4 Ndipo Mose anapfuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwacitenji anthuwa? andilekera pang'ono kundiponya miyala.