1 Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli linacoka m'cipululu ca Sini, m'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona m'Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.
2 Pamenepo anthu anatsutsana ndi Mose, nati, Tipatseni madzi timwe, Koma Mose ananena nao, Mutsutsana nane bwanji? Muyeseranji Yehova?
3 Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kucokera ku Aigupto, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu?
4 Ndipo Mose anapfuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwacitenji anthuwa? andilekera pang'ono kundiponya miyala.
5 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pita pamaso pa anthu, nutenge pamodzi nawe akuru ena a Israyeli; nutenge m'dzanja mwako ndodo ija unapanda nayo nyanja, numuke.
6 Taona, ndidzaima pamaso pako pathanthwe m'Horebe; ndipo upande thanthwe, nadzaturukamo madzi, kuti anthu amwe. Ndipo Mose anacita comweco pamaso pa akuru a Israyeli.
7 Ndipo anacha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, cifukwa ca kutsutsana kwa ana a Israyeli; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai?