1 Ndipo Yetero, wansembe wa Midyani, mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu adacitira Mose ndi Israyeli anthu ace, kuti Yehova adaturutsa Israyeli m'Aigupto.
2 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anabwera naye Zipora mkazi wa Mose (atamtuma kwao), ndi ana ace awiri;
3 dzina la winayo ndiye Gerisomu, pakuti anati, Ndakhala mlendo m'dziko lacilendo;
4 ndi dzina la mnzace ndiye Eliezere; pakuti anati, Mulungu wa kholo langa anakhala thandizo langa nandilanditsa ku lupanga la Farao.
5 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anadza ndi ana ace amuna ndi mkazi wace kwa Mose kucipululu kumene adamangako, pa phiri la Mulungu;
6 nati kwa Mose, Ine mpongozi wako Yetero ndadza kwa iwe, ndi mkazi wako, ndi ana ace omwe awiri.
7 Ndipo Mose anaturuka kukakomana ndi mpongozi wace, nawerama, nampsompsona; nafunsana ali bwanji, nalowa m'hema.