8 Ndipo anthu onse anabvomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazicita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.
9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akubvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo.
10 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zobvala zao,
11 nakonzekeretu tsiku lacitatu; pakuti tsiku lacitatu Yehova adzatsika pa phiri la Sinai pamaso pa anthu onse.
12 Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzicenjera musakwere m'phiri, musakhudza cilekezero cace; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu;
13 dzanja liri lonse lisalikhudze, wakulikhudza azimponyatu miyala, kapena kumpyoza; ngakhale coweta ngakhale munthu, zisakhale ndi moyo. Pamene lipenga libanika liu lace azikwera m'phirimo.
14 Ndipo Mose anatsika m'phiri kumka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zobvala zao.