1 Ndipo awa ndiwo maweruzo amene uziika pamaso pao.
2 Ukagula mnyamata Mhebri, azigwira nchito zaka zisanu ndi cimodzi; koma cacisanu ndi ciwiri azituruka waufulu cabe.
3 Akalowa ali yekha azituruka ali yekha; akakhala ndi mkazi, mkazi wace azituruka naye.
4 Akampatsa mkazi mbuye wace, ndipo akambalira ana amuna ndi akazi, mkaziyo ndi ana ace azikhala a mbuye wace, ndipo azituruka ali yekha.
5 Koma mnyamatayo akanenetsa, Ndikonda mbuye wanga, mkazi wanga, ndi ana anga; sindituruka waufulu;
6 pamenepo mbuye wace azifika naye kwa oweruza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wace amboole khutu lace ndi lisungulu; ndipo iye azimgwirira nchito masiku onse.