24 Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kucita monga mwa nchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao.
25 Ndipo muzitumikira Yehova Mulungu wanu, potero adzadalitsa cakudya cako, ndi madzi ako; ndipo ndidzacotsa nthenda pakati pa iwe.
26 M'dziko mwanu simudzakhala wakutaya mwana, kapena wosabala; ndidzakwaniritsa kuwerenga kwa masiku ako.
27 Ndidzatumiza kuopsa kwanga kukutsogolere, ndipo ndidzapitikitsa anthu onse amene udzafika kwao, ndipo ndidzacita kuti adani ako onse adzakuonetsa m'mbuyo mwao.
28 Ndipo ndidzatumiza mabvu akutsogolere amene adzaingitsa Ahivi, Akanani, ndi Ahiti, pamaso pako.
29 Sindidzawaingista pamaso pako caka cimodzi; kuti dziko lingakhale bwinja, ndi zirombo za kuthengo zingakucurukire.
30 Ndidzawaingitsa pang'ono pang'ono pamaso pako, kufikira utacuruka, ndi kulandira dziko colowa cako.