8 Ndipo Mose anatenga mwaziwo, nawaza pa anthu, nati, Taonani mwazi wa cipangano, cimene Yehova anacita nanu, kunena za mau awa onse,
9 Ndipo Mose ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akuru a Israyeli makumi asanu ndi awiri anakwerako;
10 ndipo anapenya Mulungu wa Israyeli; ndipo pansi pa mapazi ace panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiri, ndi ngati thupi la thambo loti mbe.
11 Koma sanaturutsa dzanja lace pa akuru a ena a Israyeli; ndipo anapenya Mulungu, nadya, namwa.
12 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m'phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi cilamulo ndi malamulo, ndawalembera kuti uwalangize.
13 Ndipo anauka Mose, ndi Yoswa mtumiki wace; ndipo Mose anakwera m'phiri la Mulungu.
14 Ndipo anati kwa akuru, Tilindeni kuno kufikira tidzabwera kwa inu; ndipo taonani, Aroni ndi Huri ali nanu; munthu akakhala ndi mlandu abwere kwa iwowa.